Malawi Broadcasting Corporation
Local Nkhani Sports

K80.4 million yapezeka pamasewero a Bullets ndi Wanderers

Ndalama zokwana K80.4 million ndi zomwe zapezeka pa masewero amu ligi ya TNM apakati pa matimu a FCB Nyasa Big Bullets komanso Mighty Mukuru Wanderers omwe aseweredwa loweruka masana pabwalo la Kamuzu.

Matimu a Wanderers komanso Bullets atenga K16.7 million timu iliyonse kuchoka pa ndalamayi (K80.4 million)

Chaka chatha, pamasewero ngati omwewa ndalama pafupifupi K67.5 million ndi zomwe zinapezeka.

Masewerowa athera 1-1 pomwe Wanderers inagoletsa kudzera mwa Isaac Kaliati ndipo Bullets inagoletsa kudzera mwa Patrick Mwaungulu.

Wolemba Praise Majawa.

Print Friendly, PDF & Email

Related posts

A Kaliati akufuna kudzapikisana nawo pa udindo wa mtsogoleri wa UTM

MBC Online

President Chakwera akhala nawo pamwambo wa mapemphero

MBC Online

Dr Usi afika mawa

Blessings Kanache
error: All Content is protected. Copyright © 2022. Malawi Broadcasting Corporation. All Right Reserved.