Mneneri Shepherd Bushiri ndi mmodzi wa atsogoleri azipembedzo omwe afika ku Mulanje, komwe mwambo wachikumbutso Cha Namondwe Freddy ukuchitikira.
Bushiri wakhala akuthandiza anthu okhudzidwa ndi Namondweyu munjira zosiyanasiyana monga chakudya, ndalama mwazina.
Masabata apitawa, iye anayamikira boma pomulola kugawa chakudya komanso kutenga nawo gawo pa chitukuko cha dziko lino.
Olemba: Blessings Cheleuka
#MBCOnlineServices