Malawi Broadcasting Corporation
Nkhani

Greenbelt Authority aiyamikira

Bungwe la National Food Reserve Agency (NFRA) komanso unduna wa zaulimi ayamikira bungwe la Greenbelt Authority kaamba ka matumba oposa 3000 a chimanga omwe awagulitsa ku NFRA.

Wapampando wa bungwe la NFRA a Dennis Kalekeni anena izi kunkhokwe za NFRA munzinda wa Lilongwe komwe amalandira chimangacho. Iwo ati nzokondweretsa kuti tsopano anthu komanso makampani akubweretsa chimanga chogulitsa kaamba koti boma linakweza mtengo wa chimanga kufika pa K750 pa kilogalamu imodzi.

A Kalekeni ati pakhala misika yoyendayenda m’madera omwe akugulamo chimanga kuti adzadzitse nkhokwezo ndi chimanga.

Poyankhulapo, mlembi mu unduna wa zaulimi a Geoffrey Mamba ati undunawu ukuchita chotheka kulimbikitsa alimi kuti asiye kudalira ulimi wamvula mmalo mwake achirimike ndi ulimi wamthilira kaamba koti mvula sikubwera modalirika.

Wachiwiri kwa wapampando wa bungwe la Greenbelt Authority, a Regina Sambakunsi, ati bungwe lao lionetsetsa kuti likuthandiza boma polima chimanga kudzera mu ulimi wamthilira kuti m’dziko muno mukhale chakudya chokwanira.

Print Friendly, PDF & Email

Related posts

Mphunzitsi ali mchitokosi atagwilira mwana

Davie Umar

Tisagulise chimanga chathu chidakali kumunda —Makwangwala

Timothy Kateta

GESD yayamba kumanga mlatho wa Limbe

Arthur Chokhotho
error: All Content is protected. Copyright © 2022. Malawi Broadcasting Corporation. All Right Reserved.