Ochita malonda pa msika wa Nsungwi ku Area 25 m’mzinda wa Lilongwe, a Emmanuel Pensulo, apereka unifolomu kwa ophunzira khumi apa sukulu ya Kalambo.
A Pensulo anati unifolomu ndi yofunika chifukwa ana amadziwika komanso kuti ana saonekera kuti akuchokera ku banja losowa chifukwa onse amavala mofanana.
Iwo anati ndi khumbo lawo kufikira ana oposa 1000 m’boma la Lilongwe ndi thandizo lomweli.
Wachiwiri kwa mphunzitsi wa mkulu pa sukuluyi, a Frotrida Kumwenda Nzimba, anati thandizoli lafika mu nthawi yake pamene ana ambiri akulephera kupita ku sukulu kaamba kosowa unifolomu.
A Nzimba anapemphanso anthu ena ofuna kwabwino kuti achitenso moteremu.