Pamene anthu ena akupitilira kusautsika ndi vuto la njala m’boma la Mangochi, Mneneri Shepherd Bushiri wapeleka chimanga kwa anthu amene amakhala pafupi ndi Goshen city ku dera la mfumu yaikulu Nankumba.
Mayi Dolasi Baluti anauza MBC kuti Ng’amba yawavuta kwabasi ndipo sakuyembekeza kuti akolora kanthu.
Iwo nathokoza a Bushiri chifukwa cha thandizoli.
Poyankhula pa sukulu ya pulaimale ya Namazizi, a Bushiri anati ndikofunika kuthandizana wina ndi mnzake zinthu zikavuta.
Mneneri wa mpingo wa ECG-Jesus Nation yu anapemphanso kampani ndi mabungwe akufuna kwabwino kuti athandize boma popereka chakudya kwa anthu.
“Inde njala yavuta, koma n’nafuna tigawane nawo anthu amene akukhala moyandikana ndi Goshen City kuti nawonso apeze chakudya.Ine sindingakwanitse kufikira aliyense, ndichifukwa chake tikuyenera kugwirana manja, “anatero a Bushiri.
Olemba Mirriam Kaliza.