Malawi Broadcasting Corporation
Local Nkhani

Feteleza wa Mbeya wasintha banja la a Thabwa modabwitsa

A Tsazo Thabwa a m’mudzi mwa Fayifi kwa mfumu yaikulu Dzoole B m’boma la Dowa akuti moyo wa pa banja lawo wasintha modabwitsa potsatira zokolora zochuluka zomwe anapeza atagwiritsa ntchito feteleza wa manyowa wa Mbeya.

Iwowa akuti anali mu umphawi wa dzaoneni, akhala akulandira mtukula pakhomo ndipo amadziwika bwino m’mudzi mwawo pochita maganyu kuti apeze thandizo la pabanja pawo.

Koma lero mkuluyu anatsekula golosale lomwe limakhala ndi katundu ochuluka komanso akuchita bizinesi yogula ndi kugulitsa mbewu, kuphatikiza ku ntchito za ulimi wa mbewu zosiyanasiyana.

Chitukukochi chinadza atalowa gulu losunga ndi kuchulukitsa ndalama la COMSIP mu cluster ya Kampanje ndipo iwo pamodzi ndi mamembala anzawo 48 anaphunzitsidwa kapangidwe ka  fetelezayu.

“Nditaphunzira kupanga fetelezayu pogwiritsa ntchito feteleza monga wa Urea, phulusa, madeya ndi ndowe, ndinakolora chimanga, fodya ndi soya ochuluka ndipo zonse pamodzi nditagulitsa ndinapeza ndalama zokwana K3.5 million,” watero Thabwa.

Ndalamayi anagwiritsa ntchito kugula malo, kumanga nyumba ndi golosale ndipo akuti amapeza ndalama zosachepera K200,000 pa tsiku.

Related posts

Kulila kwa mafoni ochuluka kwagwiritsa mbava

Alinafe Mlamba

Innovations can tackle Malawi’s challenges — Chakwera

Romeo Umali

New vehicle fleet to improve MBC’s service delivery

Romeo Umali
error: All Content is protected. Copyright © 2022. Malawi Broadcasting Corporation. All Right Reserved.