Bungwe lobwereketsa ndalama la National Economic Empowerment Fund Limited (NEEF) lati sizoona kuti lasayina mgwirizano ndi mtsogoleri wa dziko lino kuti lidzipereka ku banja lililonse ndalama zokwana K50,000 zomwe sadzabweza.
Poyankhapo pa chikalata chomwe anthu ena akufalitsa pa masamba a mchezo, Ofalitsankhani ku bungwe la NEEF, Elizabeth Mapemba, wati nkhaniyi ndi yabodza.
Mapemba wati anthu ena amaganizo oyipa ndi omwe akufalitsa bodzali pofuna kupomboneza a Malawi ponena kuti Presidential Grant 2024 ifikira mabanja onse m’dziko muno.
“NEEF imapereka ngongole motsata ndondomeko zoyikika bwino ndipo ngongole iliyonse imayenera kuti munthu abweze.
Komanso a Malawi adziwe kuti chilichose chomwe a NEEF amapanga komanso boma amachilengeza kudzera mu njira zokhazikika monga pa wailesi zoulutsa mau, zakanema komanso m’manyuzipepala,” watero Mapemba.
Iye wati akudziwa kuti pali akambelembele omwe akufuna kusocheretsa ndikubera a Malawi.