Bungwe la TRADE Programme lati chionetsero chazaulimi chomwe chinalipo sabata yatha mu nzinda wa Blantyre chakhala chopindula chifukwa alimi amene amagwira nawo ntchito apeza misika yokhazikika ya mbewu komanso zokolora zawo.
M’modzi mwa adindo ku bungweli, a Amos Simwera, ati alimiwa apeza ndalama zopyola K500 million.
A Simwera ati kupezeka kwa misika yodalilirika yotere ikulimbikitsa alimi kuti adzichita ulimi modziwiratu kuti asadzavutike kupeza kumene akagulitsire zokolora zawo.
Imodzi mwa kampani zomwe zapanga ubale ndi alimi a mtedza m’boma la Ntchisi ndiya Food Kings yomwe yati ikuyembekezera kuti alimi awagulitsa mtedza wambewu okwana ma tani 60,000.
M’modzi wa akulu akuku akampaniyi a Vilanji Nkhwazi wati alimiwa awaphunzisanso zamomwe angalimire bwino mtedza wambewu.