Malawi Broadcasting Corporation
Entertainment Local Local News Nkhani

Chionetsero cha kanema chilipo mu November

Chionetsero cha kanema cha chaka chino chichitika kumapeto a mwezi wa November munzinda wa Lilongwe, m’modzi mwa akuluakulu ku bungwe la Film Association of Malawi, a Philmon Kuipa, watsimikiza izi.

Poyankhula pa msonkhano wa olemba nkhani munzinda wa Lilongwe Lachiwiri m’mawa, iwo anati K21 million ndi imene akuyembekezera kugwiritsa ntchito pa mwambowu pamutu wakuti ‘kulimbikitsa chikhalidwe cha chi Malawi kudzera mu mafilimu’.

Kuyambira pa 29 kufika pa 30 November, kuchikonzerochi adzaonetsa mafilimu akunja komanso aku Malawi kuti anthu adzathe kusiyanitsa m’mene ntchito yopanga kanema m’dziko muno ikuyendera.

Akuipa anati kudzakhalanso mwayi ophunzitsa anthu kapangidwe kafilimu komanso kuphunzira mmene angayendetsere chuma chawo, maphunziro amene adzachititse ndi a kampani ya Old Mutual.

Aka kakhala kachitatu kuti bungwe la Film Association of Malawi lichititse mwambowu.

 

Print Friendly, PDF & Email

Related posts

Malawi thump Seychelles to reach Beach Soccer semi-finals

Norbert Jameson

Malawi commits to Mission 300

Justin Mkweu

Over 262, 000 students sit for 2024 PSLCE exams

Arthur Chokhotho
error: All Content is protected. Copyright © 2022. Malawi Broadcasting Corporation. All Right Reserved.