Malawi Broadcasting Corporation
Nkhani

Bungwe lathandiza maanja 20,000 kuthana ndi njala

Maanja oposera 20,000 kuchokera mmagulu osunga ndi kuchulukitsa ndalama omwe ali pansi pa bungwe la COMSIP akuyembekezeka kupeza zokolora zochuluka kaamba ka zipangizo za ulimi zomwe bungweli linawapatsa.

Izi zikuchitika pansi pa ntchito yolimbikitsa ntchito za ulimi ya LESP yomwe bungwe la COMSIP linapereka ndalama zokwana K1 billion ku maguluwa zomwe anagulira mbewu, feteleza ndi zipangizo zina za ulimi.

Poyankhula ndi MBC Digital, a Chikaiko Zimba, mmodzi mwa alimi omwe apindula ndi ndondomekoyi m’dela la mfumu yaikulu Chilowamatambe m’boma la Kasungu, anati iwo pamodzi ndi mamembala anzawo a Cluster ya Mkwayule akusimba lokoma pomwe apeza zokolora zochuluka chaka chino.

“Pa munda wa ekala imodzi ndi theka omwe ndinalima pogwiritsa ntchito zipangizo zaulimi zomwe ndinalandira, ndikuyembekezeka kukolora matumba okwana 70. Zaka za m’buyomu ndimakolora matumba 25 kapena 30 pa malo omwewa,” watero Zimba.

Mneneri wa bungwe la COMSIP Cooperative Union Limited, Mercy Kayuni, wati ntchito ya LESP yathandiza alimi omwe akulima mbewu monga chimanga, nyemba ndi mpunga ndipo bungwe lawo ligula zokolora zawo pa mtengo wabwino.

Mercy Kayuni, Mneneri wa bungwe la COMSIP

Boma la Kasungu ndi limodzi mwa maboma 14 omwe akupindula ndi ntchito yopititsa patsogolo ulimi ya LESP yomwe yafikira maanja omwe amalandira mtukula pakhomo ndi nthandizi wa mbwezera chilengedwe ndipo ali mmagulu osunga ndi kuchulukitsa ndalama a COMSIP.

Print Friendly, PDF & Email

Related posts

Mudzi wa aChewa autsekulira ku Lilongwe

MBC Online

Mlandu wa Bushiri wayima kaye!

Olive Phiri

BANKI YA FDH IKUYEMBEKEZERANSO PHINDU LOKWERA

MBC Online
error: All Content is protected. Copyright © 2022. Malawi Broadcasting Corporation. All Right Reserved.