Malawi Broadcasting Corporation
Local Local News Nkhani Politics

MCP ikhazikisa mfundo za chitukuko

Mtsogoleri wa dziko lino Dr Lazarus Chakwera yemwenso ndi mtsogoleri wa chipani cha Malawi Congress Party (MCP) akhazikitsa ndondomeko za mfundo za chitukuko zimene chipani cha MCP chitsatire potukula dziko lino mu zaka zikubwerazi.

Mwambo okhazikitsa mfundozi uchitika pa bwalo la zamasewero la Bingu munzinda wa Lilongwe.

Dr Chakwera akuyembekezeka kukhala nawo pa mdipiti wa anthu omwe ayende kuchokera pa Area 18 Interchange kukafika ku bwalo la zamaseweroli.

Anthu enanso otsatira chipani cha MCP ayenda kuchokera pa bwalo la Lilongwe Community, Kaunda Round about kudzera ku Crossroads komanso ku Area 49 ndi 25.

Mwambowu ukuchitika pomwe bungwe la Malawi Electoral Commission lakhazikitsa nyengo yokopa anthu pokonzekera chisankho cha pa 16 September.

Mwambo wokhazikitsa mfundowu uchika mogwirizana ndi mwambo omwe chipani cha MCP chikhazikitse kampeni yokopa anthu.

Related posts

Chitipa registers more cholera cases

Romeo Umali

Govt. promotes aquaculture to drive Malawi 2063 goals

MBC Online

Chakwera leaves for Kenya

Rabson Kondowe
error: All Content is protected. Copyright © 2022. Malawi Broadcasting Corporation. All Right Reserved.