Apolisi ku Soche mu mzinda wa Blantyre amanga Mervin Sulemani wa zaka 27 pomuganizira kuti anapha Rizwani Issa pomukhapa pa 21 mwezi uno ku Chinyonga.
Mneneri wa apolisi ya Soche, Aaron Chilala, wati Sulemani akumuganizira kuti ndi yemwe sabata yathayi, anapita ndi Issa ku nyumba ina ku Chinyonga chakumasana, kenaka atapeza kuti kulibe anthu, anakhapa ndi chikwanje Issa mpaka kumwalira, kenaka ndikuthawa pagalimoto.
Iye wati apolisi, apezanso galimoto yomwe akuganiza kuti anaigwiritsa ntchito patsikuli number yake MC 6199.
Chilala wati Sulemani wavomela kuti ndiye anapha Issa atamukakamiza kukwera galimoto yake pa Shoprite kupita ku Chinyonga komwe anamupha kenaka ndikumubera ndalama zokwana K1.5 million, cellphone komanso laptop.
Mervin Sulemani amachokera mmudzi mwa Kaleso kwa TA Mbenje ku Nsanje.