Malawi Broadcasting Corporation
Nkhani

‘Gulani katundu opangidwa mdziko muno’

Kampani ya Universal Industries yapempha anthu kuti achilimike kugula zithu zopangidwa m’dziko mommuno ndi cholinga chokweza ntchito za malonda komanso kupereka mwayi wa ntchito pakati pa aMalawi.

Mmodzi mwa akuluakulu ku kampaniyi, a Farouk Jungu, anena izi ku Mzuzu komwe amagawa katundu osiyanasiyana yemwe amapanga monga kamba, zakumwa ndi madzi kwa anthu okhala munzindawu mwaulere.

“Ifeyo timadalira makasitomala komanso amalonda omwe amatigula ndinso kugulitsa katundu wathu amene timapanga mdziko momwe muno, polimbikitsa ntchito za malonda adziko muno,” watero Jungu.

Mmodzi mwa anthu omwe analandira katunduyu, a Andrew Jere, anayamikira a Universal Industries chifukwa cha katundu wabwino yemwe akuti kampaniyi ikupanga ndipo analimbikitsa anthu kuti adzigula katundu opangidwa m’dziko muno.

Olemba: George Mkandawire

Print Friendly, PDF & Email

Related posts

Achewa athira nsembe

MBC Online

Ana 169 apulumutsidwa ku maukwati

Lonjezo Msodoka

Akuba osawutsa pa msewu wa ABC anjatidwa

Romeo Umali
error: All Content is protected. Copyright © 2022. Malawi Broadcasting Corporation. All Right Reserved.