Apolisi ku Lilongwe amanga a James Paulo, 35, kaamba kobera anthu ndalama ndi katundu monga lamya za m’manja pogwiritsa ntchito njira yotchedwa Chimtambala.
Mu njirayi, a Paulo amatenga mapepala olembapo ndi kuwadula mofanana ndi ndalama kenako amawamanga pamodzi ngati mpukutu wandalama ndipo m’mapeto amaikamo ndalama kuti mpukutu wonsewo udziwoneka ngati ndalama.
Ofalitsankhani ku Polisi ya Lilongwe, a Hastings Chigalu, ati a Paulo akaona munthu amaponya mpukutuwo pansi ndikuuza munthuyo kuti watola ndalama ndipo akagawane ndipo akapita kogawanako, amapezerapo mpata womubera munthuyo.
Paulo, yemwe anamangidwaponso pamlandu ngati womwewu, amachita izi pamlatho wa Lilongwe.
Iye amachokera m’boma la Zomba.