Malawi Broadcasting Corporation
Local Nkhani

Amugwira akuba ma mita a Water Board

Apolisi ku Zomba amanga Patrick Mbiri wazaka 26 pomuganizira kuti waba mamita a madzi a bungwe la Water Board komanso zotsegulira madzi.

Mneneri wapolisi ku Zomba, Patricia Sipiliano wati apolisi akhala akulandira malipoti akuti anthu ena akumaba mamita komanso zipangizo zina za bungweli mtawuni ya Zomba ndi madera ozungulira monga Chinamwali.

Apolisi atachita kafukufuku, anamupezelera Mbiri akuba zotsegulira madzi kapena kuti ma tap kudera la Sogoja ku Matawale.

Mbiri, yemwe amachokera mmudzi wa Kazembe, mfumu yaikulu Chikowi ku Zomba, wavomera kuti wakhala akuba zipangizozi.

Print Friendly, PDF & Email

Related posts

Cost of housing is expensive in BT, MZ — CFSC

Olive Phiri

Heatwave to hit parts of Malawi — MET

Chisomo Break

Walipira chindapusa chifukwa chonyoza wodwala AIDS

Charles Pensulo
error: All Content is protected. Copyright © 2022. Malawi Broadcasting Corporation. All Right Reserved.