Malawi Broadcasting Corporation
Local Nkhani

Atsiriza kufufuza za imfa ya anthu asanu ku Blantyre

A polisi ati katswiri opima matupi aanthu, Charles Dzamalala, watsiriza kupima matupi a anthu omwe  afa atamwa mowa wina kwa Manase ku Blantyre.

Mneneri wa apolisi mchigawo chakummwera, Joseph Sauka, wati zotsatirazi azitulutsa nthawi ina iliyonse.

A Sauka ati anthu asanuwa anamwalira mmodzi mmodzi atamwa mowawu, zomwe zinachititsa achipatala kuyamba ayimitsa kuti awiri mwa matupi a anthuwo asawaike mmanda kuti awapime kaye.

Anthu omwe anamwa mowawu, malinga ndi a Sauka, analipo asanu ndi atatu ndipo awiri ali mwakayakaya pomwe mmodzi akuwonetsa kusintha.

 

Related posts

CHAKWERA LEADS MALAWIANS IN MOURNING JZU

MBC Online

MBC rolls out Ngwe Ngwe Ngwe project open days

Rabson Kondowe

WHEN FLOODS STRIKE

Yamikani Simtowe
error: All Content is protected. Copyright © 2022. Malawi Broadcasting Corporation. All Right Reserved.