Malawi Broadcasting Corporation
Crime Local Local News Nkhani

‘Mukapezeka ndi Chamba mumangidwa’

Apolisi ku Karonga achenjeza kuti aliyense opezeka ndi fodya wamkulu (Chamba) adzimangidwa.

Iwo anena zimenezi atamanga a Michael Chiwaya azaka 31 powaganizira kuti apezeka ndi Chamba cha makilogiramu 38 mosavomerezeka ndi boma.

Ofalitsankhani ku polisi ya Karonga, a Margret Msiska, ati oganiziridwayu pa 09 October 2024 anapezeka ndi zikwama zitatu ndi thumba la pulasitiki pa njinga zomwe akuti zimaoneka mokayikitsa ndipo wapolisi yemwe anaona izi anayamba kufufuza ndipo anapeza chambachi.

A Chiwaya aonekera kubwalo la milandu posachedwepa poyankha mlandu opezeka ndi chamba popanda chilolezo.

Iwo amachokera m’mudzi wa Mpeta kudera la Mfumu Kamphambale m’boma la Nkhotakota.

 

Related posts

First Lady calls for more financing of women empowerment programmes

Romeo Umali

Maso Awards partners Ad City for 2024 ceremony

Romeo Umali

Climate Smart Programme participants receive wages

Romeo Umali
error: All Content is protected. Copyright © 2022. Malawi Broadcasting Corporation. All Right Reserved.