Malawi Broadcasting Corporation
Floods Local News Nkhani

Anthu sakumvetsa madzi ataphulika mu shop

Anthu okhala kwa Jumbe ku Machinjiri ati sakumvetsa kuti anamanga malo awo ochitira malonda pamwamba pa paipi yaikulu yamadzi a Blantyre Water Board, katundu ochuluka ataonongeka madzi ataphulika pamalowo.

Pakadali pano, a Blantyre Water Board ali mkati kukonzanso paipiyi, madzi omwe anayenda ngati namondwe atasakaza katundu wandalama zochuluka mu shopuyi.

Mwini malowa, a Guest Tambala, ati nawo mutu waima kamba koti sakumvetsa chomwe chachitikachi.

Olembankhani wathu wati mu shopuyi muli chidzenje chomwe chakumbika ndi madzi ophulikawa, pomwe ogwira ntchito ku BWB akuyesera kukonzanso paipiyi.

Olemba: Mphatso Tebulo

Related posts

Judiciary, MBC partner for open justice

Secret Segula

NRB impressed on first day of birth registration

Romeo Umali

Matupi ena angozi ya ndege awaika m’manda masanawa

Romeo Umali
error: All Content is protected. Copyright © 2022. Malawi Broadcasting Corporation. All Right Reserved.