Boma, kudzera ku unduna oona za maubale a dziko lino ndi maiko akunja, lati likufufuzabe malipoti akuti aMalawi ena amwalira pa ngozi ya nyumba yosanjikana imene yagwa m’dziko la South Africa.
Ofalitsankhani ku undunawu, a Charles Nkhalamba, ati akuchita kafukufuku kudzera ku ofesi ya kazembe wa dziko lino ku South Africako.
Nyumbayi idagwa m’dera la George ndi kupha anthu asanu ndi atatu. Anthu 81 ndi amene akuganiziridwa kuti anali pamalopo.