Malawi Broadcasting Corporation
Local Nkhani

Anthu ayamikira ntchito zabwino za Kapusa

Malemu Geoffrey Kapusa waikidwa mmanda lero kumudzi kwawo.

Anthu osiyanasiyana anali nawo pa mwambowu, ndipo onse anati Geoffrey wasiya mbiri yotamandika pankhani zoulutsa mawu pakanema m’dziko muno.

Geofrey “Mr Splash” Kapusa anamwalira dzana pachipatala cha Queen Elizabeth Central mu mzinda wa Blantyre.

Iye anadziwika kwambiri ndikuthandiza oyimba kuti adziwike kudzera mu programme yake ya Music Splash pa kanema ya MBC, kuyambira pomwe inkayamba kumene ngati TVM.

Geoffrey, yemwe anabadwa m’chaka cha 1971, wasiya ana atatu.

Related posts

NYALONJE URGES WOMEN TO REPORT SEXUAL ABUSE IN WORKPLACES

Romeo Umali

UTM ilingalire mozama — Mwakasungula

Romeo Umali

CELEBRATE RESPONSIBLY TO AVOID POST-VALENTINE’S DAY STRESS — FPAM

Romeo Umali
error: All Content is protected. Copyright © 2022. Malawi Broadcasting Corporation. All Right Reserved.