Malawi Broadcasting Corporation
Nkhani

Amumanga ataba mbendera yadziko

Apolisi ku Mulanje amanga Shadreck Medson wazaka 22 pomuganizira kuti waba mbendera zadziko zokwana zisanu ndi imodzi – 6 kwa Nkhonya m’boma la Mulanje.

Ofalitsankhani zapolisi ku chigawo cha kummwera, a Edward Kabango, wati pakadali pano, apolisi akufufuza anthu ena awiri amene akuwaganizira kuti anaba nawo mbenderazo.

Malinga ndi a Kabango, anthuwo anaba mbenderazo, zomwe zinayikidwa m’mbali mwa msewu wopita ku bwalo la zamasewero la Mulanje Park kumene kunali mwambo wokumbukira anthu omwe anamwalira kamba ka namondwe wa Freddy.

Mwambowo utatha, atatuwo anapita kukaba mbenderazo limodzi ndi mitengo yomwe kunamangidwa mbenderazo, zomwe ndi za ndalama pafupifupi K540,000.

Medson ndi wa mmudzi wa Ngutuma, mfumu yaikulu Chikumbu m’boma la Mulanje.

Related posts

Ngozi za kabaza zikuchulukirabe

Rabson Kondowe

MEC ionjezera masiku m’gawo loyamba la kalembera

Rabson Kondowe

Prezidenti Chakwera acheza ndi anthu pa Nanyumbu ku Machinga

Rabson Kondowe
error: All Content is protected. Copyright © 2022. Malawi Broadcasting Corporation. All Right Reserved.