Boma ladzudzula m’chitidwe omwe anthu ena akumachita otenga ziphaso za unzika za anthu ena powanamiza kuti awamangira nyumba, mwa zina.
Nduna yofalitsa nkhani, a Moses Kunkuyu, atsindikiza izi lero mu mzinda wa Blantyre komwe anati boma likhazikitsa zilango zokhwima zomwe zidzagwire ntchito kwa aliyense opezeka olakwa.
Iwo ati m’chitidwewu ndi osavomerezeka ndipo aMalawi akhale tcheru ndikukaneneza ku Polisi onse amene akuchita izi.
Olemba: Timothy Kateta