Malawi Broadcasting Corporation
Nkhani

A Dossi ayikidwa m’manda ndi mwambo wachisilikali

Mwambo oyika m’manda malemu Moses Dossi, omwe anaakhalapo olembankhani za masewero komanso nduna ya zamasewero mu ulamulo wa boma la chipani cha United Democratic Front, uli mkati m’mudzi mwa Kalimanjera kwa Chapananga m’boma la Chikwawa.

Mtsogoleri wa dziko lino, Dr Lazarus Chakwera, walamula kuti malemu Dosi ayikidwe m’manda motsatira mwambo wa chisilikali popereka ulemu ku ntchito zawo.

Nduna yoona zamalo, a Deus Gumba, ndi amene akuyimilira prezidenti wa dziko lino.

A Dossi anamwalira lachinayi mmawa atadwala kwa nthawi yayitali.

Related posts

Drones in the Air at Chikangawa

Romeo Umali

Ayamikira Dr Chakwera posankha mabodi atsopano a kampani zaboma

Rabson Kondowe

MRCS yamaliza kuthandiza okhudzidwa ndi namodwe Judy ku Phalombe

Secret Segula
error: All Content is protected. Copyright © 2022. Malawi Broadcasting Corporation. All Right Reserved.