Malawi Broadcasting Corporation
Local Nkhani

A Chakwera acheza ndi ochita malonda kunyumba ya boma

Mtsogoleri wa dziko lino, Dr. Lazarus Chakwera, masana ano akuyembekezeka kucheza ndi ochita malonda ochokera mmisika yosiyanasiyana ya  kuchigawo chakummawa kwa dziko lino.

Ochita malonda osachepera 300 ndiwo afika kunyumba ya boma ya Chikoko Bay ku Mangochi.

Mwazina, Dr. Chakwera akufuna kumva ena mwa mavuto amene anthuwa akukumana nawo komanso kupeza ena mwa mayankho a mavutowo.

Ena mwa ochita malondawa achokera ku misika ya ku Zomba, Machinga-Ntaja, Nsanama, Liwonde, Mangochi ndi misika ina.

 

Olemba: Mirriam Kaliza

Related posts

NBS takes executive and private banking to Zomba

Rabson Kondowe

Language barriers hindering the deaf — MANAD

Rabson Kondowe

Habitat for Humanity brings hope to Cyclone Freddy survivors

Romeo Umali
error: All Content is protected. Copyright © 2022. Malawi Broadcasting Corporation. All Right Reserved.