Malawi Broadcasting Corporation
Local Nkhani

Ifenso tikuthandiza pa ntchito zokopa alendo —Daza

Mmodzi wa anthu  ochita malonda ogulitsa zakudya zophika zachi Malawi a Aubrey Daza, amene ndi mwini wa malo odyera a Chanza Take Away m’boma la Ntcheu, wati nawo amalonda ang’ono ang’ono mgawo  lawoli akuthandiza pantchito  zokopa  alendo.

Iwo anena izi pomwe mwezi uno, dziko lino likukumbukira ntchito zokopa alendo.

A Daza ati pakadali  pano, a Malawi ambiri anamvetsesa ubwino wa kudya  zakudya zachikhalidwe, zimenenso zikuchititsa kuti ntchito zawo ngati amalonda zidziyenda bwino.

Mmodzi mwa anthu amene tinakumana nawo pa malowa, a Julius Phiri, amene anali pa ulendo ochokera mu mzinda wa Mzuzu, anati ndiokhutira ndi momwe malo ang’ono ang’ono ngati otere akulimbikitsira ntchito zokopa alendo pogulitsa zakudya zachiMalawi.

 

Wolemba: Geoffrey Chinawa ndi Chisomo Break

Related posts

Govt to upgrade health centers

Romeo Umali

Teenager punished for escaping police custody

Romeo Umali

Climate Smart Programme participants receive wages

Romeo Umali
error: All Content is protected. Copyright © 2022. Malawi Broadcasting Corporation. All Right Reserved.