Malawi Broadcasting Corporation
Culture Local News Nkhani Politics

Inkosi M’mbelwa yadzudzula ndale zonyozana

Inkosi ya Makhosi M’mbelwa V yati aMalawi akuyenera kupewa m’chitidwe wa ziwawa chifukwa dziko lino limakonda mtendere.

Inkosiyi imayankhula izi pa mwambo wa Umthetho ku Hora m’boma la Mzimba.

Mfumuyi inalangizanso zipani zonse za ndale ndi owatsatira, pamene masiku azisankho aluyandikira, kuti apewe ndale zonyozana chifukwa sizingamange dziko lino.

Mfumuyi inatinso iyi ndi nthawi yomwe aMalawi akuyenera kugwirana manja poonetsetsa kuti m’fundo zomwe boma linalonjeza zikukwaniritsidwa.

Olemba: Jackson Sichali

Related posts

Chakwera akhala nawo pa Misa ya mayi Shanil Dzimbiri

MBC Online

Maintain human agency at centre of technological advancements – DC

Rabson Kondowe

Senga Hills tourism development to boost rural income

Romeo Umali
error: All Content is protected. Copyright © 2022. Malawi Broadcasting Corporation. All Right Reserved.