Malawi Broadcasting Corporation
Local Nkhani

Dzaomboleni galimoto zanu, atero a MRA

Bungwe lotolera misonkho la Malawi Revenue Authority (MRA) lalangiza anthu amene ali ndi galimoto zawo pachipata cha Songwe Border Post kuti akaombole galimotozi ati chifukwa chakuti zikutha malo pamalowa.

Mmodzi wa akuluakulu ku bungweli, a Steven Kapoloma, ati pamalowa pali galimoto zambiri.

“Anthu ambiri anagula galimoto kunja ndipo zitafika akulephera kuwombola, zomwe zikuchititsa kuti malo ano adzadze galimotozi,”  a Kapoloma anafotokoza.

Iwo anapempha anthu kuti adzifufuza bwino bwino patsamba lawo ndikuwerengera ndalama zimene zikufunikira kuti awombole galimoto yawo asanayitanitse.

A Kapoloma alangiza anthu kuti atengere mwayi wadongosolo loti akhoza kumalipira ndalama zowombolerazi pang’onopang’ono akangoyitanitsa kuti asamapanikizike.

 

Olemba: Henry Haukeya

Related posts

Chakwera courts investors in rail sector

MBC Online

‘Malawi ali ndi kuthekera kochita bwino payekha’

Rabson Kondowe

Mohammad Mokhber ndi mtsogoleri wa dziko la Iran

Romeo Umali
error: All Content is protected. Copyright © 2022. Malawi Broadcasting Corporation. All Right Reserved.