Mkulu wa bungwe lowulutsa mawu la Malawi Broadcasting Corporation (MBC), a George Kasakula, ati bungwe lawo lidzagwira ntchito mwaukadaulo ndi mopanda kukondera pa chisankho cha chaka cha mawa.
A Kasakula anena zimenezi ku Lilongwe pa zokambirana zokhudza ndondomeko zomwe bungwe la MBC lakonza zothandiza kuti lidzatumikire aMalawi popanda vuto.
Pa msonkhanowu pali alembi a zipani zosiyanasiyana monga MCP, DPP, UDF, Aford ndi zina zambiri komanso wapampando wa bungwe la atolankhani la Misa.