Yemwe anali mlendo olemekezeka pa mwambo owonetsa kanema wa Justice ku Lilongwe a Dalitso Kabambe wapempha a Malawi kuti aziikapo chidwi potukula aluso a mdziko muno.
A Kabambe anena izi pomwe ati mdziko muno muli aluso osiyanasiyana omwe mbali yawo akuyesetsa koma akufunikira thandizo.
“Mdziko muno muli luso ndipo kanemayi ndi umboni oti a Malawi tikukula pankhani zaluso. Zatsala kwa ife tsopano a Malawi kuti tiwapatse zoyenera alusowa kuti apitilize kutisangalatsa,” anatero a Kabambe.
M’mawu ake mkulu wa kampani ya Magic Promotions, Brazio Mathias, yemwe walemba ndikujambula kanemayi wati ndiokondwa poti pang’onopang’ono a Malawi akuvomereza kuti mdziko muno muli luso.
Iye watinso anthu okhala m’mizinda ina asadandaule poti akhala akulowera komweko kukaonetsanso kanemayi.