Nduna yoona za madzi komanso ukhondo, mayi Abida Mia, pamodzi ndi anthu ena ambiri, asonkhana ku Machinjiri Area 3 mu mzinda wa Blantyre kumene akukhuza maliro a bambo Geoffrey Kapusa.
Malemu Kapusa anali m’modzi wa anthu odziwika bwino poulutsa mawu ndipo anadziwika ndi programme yotchedwa ‘Music Splash’ pa kanema wa MBC m’zaka zapitazo.
Kumene kuli zovutaku kukhala mwambo wa mapemphero kenako maliro anyamulidwa kupita ku mudzi wa Mkanda ku Malosa m’boma la Zomba komwe akawayike m’manda lachinayi.
Iwo amwalira m’banda kucha wa lero pa chipatala cha Queen Elizabeth.
#MBCDigital
#Manthu