Malawi Broadcasting Corporation
Nkhani

Ulendo wotsiriza wa Dr Chilima wayambika kupita ku Nsipe

Galimoto yomwe yanyamula malemu Dr Saulos Chilima kubwalo lazamasewero la Bingu National lanyamuka pa mdipiti kupita kumudzi kwawo kwa Mbirimtengerenji mdera la mfumu yaikulu Champiti ku Nsipe m’boma la Ntcheu.

Prezidenti wa dziko lino, Dr Lazarus Chakwera komanso mayi wa dziko lino Madam Monica Chakwera ndiwo anatsogolera mtundu wa a Malawi popereka ulemu wotsiriza kwa malemu Dr Chilima.

Thupi la Malemu Dr Chilima akaliyika m’manda mawa Lolemba, lomwe a Prezidenti a dziko lino akhazikitsa kuti likhale tsiku la tchuthi.

Related posts

‘Nyumba yamalamulo ya ana ikufunika thumba lapadera’

Romeo Umali

Amangidwa powaganizira kuti anapha munthu

Romeo Umali

Asilikali akufunafunabe ndege yomwe inanyamula wachiwiri kwa mtsogoleri wadziko lino ku Chikangawa

MBC Online
error: All Content is protected. Copyright © 2022. Malawi Broadcasting Corporation. All Right Reserved.