Malawi Broadcasting Corporation
Local Nkhani

Mwana wa a Chilima wati munthu amafa pomwe anthu amuiwala

Zimakhala zovuta kuti mwana kawirikawiri alankhule pa maliro a bambo ake kapena mayi ake. Zimenezi zikachitika nthawi zambiri zimathera misozi.

Zimene wachita Sean Chilima, mwana wa mwamuna wa malemu Dr Saulos Chilima, zaonetsa poyera kuti ndi wolimba mtima komanso wodzipereka pochita zinthu.

Poyankhula ku khwimbi la anthu lomwe lasonkhana kubwalo laza masewero la Bingu National, Sean anati adaphunzira zambiri kuchokera kwa bambo ake.

Iye anati bambo ake amakonda kukhala bwino ndi anthu komanso amakonda kupemphera.

“Bambo anga akafuna chinthu amachikwaniritsa ndipo ndinaphunzira zambiri kwa iwo kufika pano,” anatero Sean.

Iye anati munthu amafa pokhapokha ngati anthu amuiwala ndipo anati akudziwa kuti anthu adzawakumbukira bambo ake mpaka mibadwo yamtsogolo chifukwa cha zomwe adachita ku dziko lino.

Iye wati adzawakumbukira bambo ake chifukwa choti amawakonda kwambiri ndi mayi ake a Mary Chilima.

Print Friendly, PDF & Email

Author

  • Mayeso Chikhadzula joined MBC in 2006, he's an Investigative Journalist and Principal Reporter. He's also a News Anchor, Presenter, and producer.

Related posts

Maranatha Academy rewards form four students with flight experience

McDonald Chiwayula

Tobacco rakes in $53.7 million

Justin Mkweu

Scorchers lero imwemwetera

Paul Mlowoka
error: All Content is protected. Copyright © 2022. Malawi Broadcasting Corporation. All Right Reserved.