Osewera masewero othamanga anayi amene ali ndi ulumali osaona akhala akupita m’dziko la France posachedwapa kuti akapikisane nawo ku mpikisano wa 2024 Paris Paralympic.
Nduna ya zamasewero, a Uchizi Mkandawire, anati boma ndi lokondwa kaamba kakuti osewerawa akupita ku mpikisanawu atatsatira ndondomeko zonse kusiyana ndi nthawi zonse pomwe osewera anangoyitanidwako pongowamvera chisoni.
A Mkandawire amayankhula izi pa mwambo otsanzikana ndi osewerawa mu mzinda wa Lilongwe.
Mtsogoleri wa bungwe la Malawi Paralympic Committee, a James Chiutsi, anati izi zikutheka potsatira ndondomeko yawo yomwe anakonza kuti dziko lino likhare ndi osewera akhupsya oti akapikisane nawo pa mpikisano wa dziko lonse omwe udzachitike mu chaka cha 2028 ku Los Angeles m’dziko la America.
A Chiutsi ati ichi ndi chiyambi chabe chifukwa zambiri zabwino zichitika.