Malawi Broadcasting Corporation
Crime Development Local Local News Nkhani

Ukayidi wa zaka zitatu ataba ng’ombe ya Eid

Khothi la Midima ku Limbe mu mzinda wa Blantyre lagamula kuti a Chikondi Maluwa, 23, akagwire ukayidi kwa zaka zitatu ataba ng’ombe ya anthu ena omwe anakonza kuti adzayiphe pa chikondwelero cha Eid ya 2025.

Ofalitsankhani pa Polisi ya Limbe, a Aubrey Singanyama, ati a Maluwa anaba ng’ombeyo ku Mpingwe mu mzinda omwewu.

A Singanyama ati mu bwalo la milandu, a Malawa anapempha kuti alandire chilango chofewa chifukwa sanavute kuvomereza mlanduwu.

Koma oweluza milandu anaperekabe zaka zitatuzo pofuna kupereka phunziro kwa ena amene akhoza kuchita zomwezi.

Chikondi Maluwa ndi wa m’mudzi wa Tsoka, m’dera la mfumu yayikulu Thomas m’boma la Thyolo.

 

Related posts

14 arrested for armed robbery in Lilongwe

Rabson Kondowe

Tithandizane kulimbana ndi khansa ya chiberekero — Chiponda

Romeo Umali

RBM OPTIMISTIC OF CONTAINING INFLATION

Rabson Kondowe
error: All Content is protected. Copyright © 2022. Malawi Broadcasting Corporation. All Right Reserved.