Malawi Broadcasting Corporation
News Nkhani

Tiyeni tilange ana moyenera —Bushiri

Mneneri wa mpingo wa Enlightened Christian Gathering (ECG), Shepherd Bushiri, wadzudzula mchitidwe olanga ana mopitilira muyeso akalakwitsa, ponena kuti izi ndi nkhanza.

Iwo anena izi pamene amagulira katundu osiyanasiyana mwana  wa mmudzi mwa Mndola, Mfumu yaikulu Kambwiri m’boma la Salima, amene anadyetsedwa dowe wamuwisi ochuluka masiku apitawa atagwidwa akuba m’munda.

Mneneriyu wati nkhani ya mwanayu ndiyomvetsa chisoni ndipo walonjeza kuti amuthandiza kuti achite maphunziro ake ndikudzakhala mzika yodalirika.

Katundu yemwe amugulirayu ndikuphatikizapo zovala,nsapato komanso zofunda.

Anthu osiyanasiyana, kuphatizikapo bungwe la Malawi Human Rights Commission, adzudzula amene anachitira nkhanza mwanayu ndipo apempha boma kuti lilowelerepo.

Related posts

NRB yalemba anthu opyola 12 million

Alinafe Mlamba

Man sentenced to 21 years in jail for murder, robbery

Romeo Umali

PCL, former employees court case adjourned to tomorrow

Rabson Kondowe
error: All Content is protected. Copyright © 2022. Malawi Broadcasting Corporation. All Right Reserved.