Malawi Broadcasting Corporation
News Nkhani

Adzudzula aphungu kamba kosapereka ulemu kwa Sipikala

Mmodzi mwa akuluakulu a chipani cha MCP ku nyumba ya malamulo,  a Ulemu Chilapondwa, adzudzula aphungu anyumba ya malamulo kamba ka khalidwe losapereka ulemu kwa Sipikala wa nyumba ya malamulo a Catherine Gotani Hara.

A chilapondwa, omwe ndi phungu wadera la Ntchisi South, anadandaula kuti atatulutsidwa mnyumbayi lachitatu sabata yatha, phungu wadera la Rumphi East, a Kamlepo Kalua, anakalankhula mawu onyoza sipika wanyumbayi pa masamba amchezo.

Poyankhapo pankhaniyi, mtsogoleri wazokambirana mnyumba ya malamulo, a Richard Chimwendo Banda, adandaula komanso kudzudzula  khalidwe limene adadonyeza a Kalua, yemwe akuti adanyoza mayi Catherine Gotani Hara polankhula ndi atolankhani sabata yatha.

Wachiwiri kwa sipika wanyumba yamalamulo, a Madalitso Kazombo, anatsindika kufunika kopeleka ulemu kwa mtsogoleri wanyumbayi yemwe ndi sipikala, ponena kuti malamulo a nyumbayi amafotokoza momveka bwino pa nkhani ya ulemu kwa atsogoleri.

Print Friendly, PDF & Email

Related posts

LCC warns on sand mining

MBC Online

Bullets restock replica jersey

MBC Online

Good start for Moyale

Rudovicko Nyirenda
error: All Content is protected. Copyright © 2022. Malawi Broadcasting Corporation. All Right Reserved.