Ena mwa anthu 2000 opindula
Mtsogoleri wa Mpingo wa Salvation for All Ministries International, Apostle Clifford Kawinga, wati ulimi wa mthilira ungathandize dziko lino kukhala lodziyimira palokha pachakudya.
Apostle Kawinga anena izi pamene amagawa matumba a ufa komanso kulalikira uthenga wa Mulungu kwa nyezelera m’boma la Phalombe.
Iwo ati kusintha kwa nyengo kuphunzitse aMalawi kuyamba kupanga ulimi wamakono.
A Kawinga apempha mabungwe ndi mipingo kuti agwirane manja pothandiza anthu amene akhudzidwa ndi njala m’dziko muno.
Poyankhulapo, Paramount Chief Kaduya yati boma la Phalombe lakhudzidwa kwambiri ndi njala ndipo apempha akufuna kwabwino kuti athandize.
Olemba Blessings Cheleuka.