Malawi Broadcasting Corporation
Local Local News Nkhani

Apolisi abalalitsa anthu omwe amachita zipolowe pa mpingo wa CCAP wa Mibawa ku Mbayani

Apolisi aponya utsi okhetsa misonzi pobalalitsa anthu omwe anayambitsa zipolowe ku tchalitchi ya mpingo wa CCAP ya M’bawa ku Mbayani mu mzinda wa Blantyre.

Izi zinachitika potsatira kusamvana komwe kunabuka pakati pa akuluakulu a mpingowu ndi achibale a munthu wina yemwe wamwalira koma akuti anali membala wa mpingowu.

Malingana ndi mkulu owona zachitetezo ku bungwe la MBC yemwe anawona izi zikuchitika, a Ekaby Chikaphupha, malipoti akusonyeza kuti nkanganowu unabuka pomwe akuluakulu a mpingo anakana kuti sayimbira maliro a malemuwo ngakhale ali mkhristu wawo chifukwa chakhalidwe lake lopapira mowa mwa uchidwakwa.

Izi zinadzetsa mkwiyo kwa achibale amalemuyu komanso ena omwe amakhala mozungulira derali, zomwe zinapangitsa kuti ayambitse chipwilikiti poyamba kugenda komanso kufuna kutentha tchalitchili chifukwa chokana mkhristu wawo.

Powona izi, mpamene akuluakulu ampingowo anayimbira lamya apolisi ya Mbayani omwe anathamanga ndikudzaponya utsi okhetsa misonzi pofuna kubalalitsa anthu omwe amatsogolera zipolowezi.

Padakali pano,akuluakulu a mpingo wa CCAP wa Mibawa sanathilirepo ndemanga pa nkhaniyi.

 

Related posts

KYUNGU DRUMS UP SUPPORT FOR KACP CULTURAL HERITAGE FESTIVAL

MBC Online

Standard Bank Malawi for empowered HR Managers

Romeo Umali

Former bank teller nabbed for robbing ex-girlfriend at work

Romeo Umali
error: All Content is protected. Copyright © 2022. Malawi Broadcasting Corporation. All Right Reserved.