Malawi Broadcasting Corporation
Agriculture Development Local Local News Nkhani

‘Tikufuna changu pantchito zachitukuko’

Wachiwiri kwa nduna yoona za ulimi, a Benedicto Chambo, wapereka mwezi umodzi ku kampani ya Sawa Group kuti ikhale itamaliza ntchito yomanga nyumba ya Water Users Association (WUA) m’boma la Dowa.

A Chambo amayankhula izi pamene amayendera chitukuko cha ulimi wa mthilira pansi pa Programme For Rural Irrigation Development Programme (PRIDE) ndi thandizo lochokera kubungwe la IFAD ndi boma la Malawi.

“…boma lidawapatsa chilichonse koma akulephera kuchita zomwe anzawo achita,” a Chambo amatero.

Iwo ayamikira kampani ya FISD, yomwe ikumanga Dowa Dambo 2 Irrigation Scheme kumene alimi oposa 2,000 akuyenera kupindula.

Ndalama zokwana K9.9 billion ndi zimene zikugwira ntchito yomangira ma dam pa ulimi wa mthilira kwa Chakhaza m’boma la Dowa pamene madzi ena adzigwiritsa ntchito ngati akumwa.

Ntchito ya ulimi wamthilira ya Dowa Dambo 1 irrigation scheme yomwe akumanga a Sawa Group ndi ya K8.2 billion.

Print Friendly, PDF & Email

Author

  • Mayeso Chikhadzula joined MBC in 2006, he's an Investigative Journalist and Principal Reporter. He's also a News Anchor, Presenter, and producer.

Related posts

Chakwera akhala nawo pa Misa ya mayi Shanil Dzimbiri

MBC Online

Police, Mzuzu residents strengthen ties through community hike

MBC Online

Chakwera Calls for Robust Regional Integration

Alick Sambo
error: All Content is protected. Copyright © 2022. Malawi Broadcasting Corporation. All Right Reserved.