Mabungwe amene si aboma m’dziko muno apempha aMalawi kuti asiye m’chitidwe ogwiritsa ntchito mapepala opyapyala amene amapezeka pa msika, pamene nkhaniyi idakali ku bwalo la milandu.
M’modzi mwa adindo aku Lilongwe Wildlife Trust, a Dorothy Tembo Nhlema, anena izi ku Lilongwe pamsokhano wa olemba nkhani kumene amafotokoza nkhani yokhudza chiletso chimene kampani zopanga mapepala oterewa zidatenga motsutsana ndi boma komanso mabungwewa.
Kampanizi zati zikufuna bwalo lalikulu lamilandu liunike ngati ndikolakwika kupanga mapepalawa.
A Nhlema ati mapepala opyapyala amapereka chiopsezo ku umoyo wa anthu komanso chilengedwe.
M’modzi mwa akuluakulu ku bungwe la CISONEC, a Julius Ng’oma, apempha office ya mlangizi waboma pankhani zamalamulo kuti ithandizire kuchotsa chiletso chimene kampani zopanga mapepalawa zinanatenga.