Nduna ya zokopa alendo, a Vera Kamtukule, yalimbikitsa anthu m’dziko muno kuti adzigwira ntchito limodzi ndi akatswiri a zachilengedwe pa ntchito yobzyala mitengo.
A Kamtukule ati izi ndi zofunika kaamba kakuti mitengo imafunika chisamaliro ikamakula, potwngeranso kuti anthu amadzala mitengo 10 million pa chaka koma 100,000 yokha ndiyo imakula.
Izi zinadziwika pa ntchito yobzyala mitengo kudera la mfumu yayikulu Maganga m’boma la Salima.