Malawi Broadcasting Corporation
Local Nkhani

Tatumiza akatswiri woulutsa ma Drone — MUST

Chinthuzi: UNICEF

Sukulu ya za ukachenjede ya Malawi University  of Science and Technology (MUST) yatumiza akatswiri oulutsa tindege touluka tokha mlengamlenga kuti akathandize ndi ntchito yofunafuna ndege yomwe wakwera  wachiwiri kwa mtsogoleri wa dziko lino, Dr Saulos Chilima ndi anthu ena.

Ofalitsankhani wasukuluyi, a James Mphande, wauza MBC kuti tindegeti, tomwe timadziwika kuti ma Drones mchingerezi, tilipo toposa tisanu ndipo tikathandiza kwambiri chifukwa tidzikajambula dera lalikulu kwambiri mukanthawi kochepa.

A Mphande ati akatswiriwa anyamuka lero madzulo kupita m’chigawo chakumpoto.

Ndege yomwe wakwera wachiwiri kwa mtsogoleri wa dziko linoyu, yomwe inabwelera italephela kutera pa bwalo la ndege la Mzuzu, akuyiganizira kuti yasowa mu nkhalango ya Chikangawa chifukwa cha kuipa kwa nyengo.

 

 

Related posts

A Bango ayamika Dr Chakwera chifukwa choganizira anthu a m’boma la Kasungu

Mayeso Chikhadzula

Gestational Diabetes likely among expectant mothers, study reveals

Romeo Umali

ULADI MUSSA ATHOKOZA DR CHAKWERA

MBC Online
error: All Content is protected. Copyright © 2022. Malawi Broadcasting Corporation. All Right Reserved.