M’modzi mwa akatswiri oyimba nyimbo za Hip-hop komanso katakwe paza Graphic Designing, Kennedy Mwenya, yemwe amatchuka kuti Spiral, wamwalira pangozi ya galimoto ku Mzuzu.
Malipoti akuti iyeyu anapita ku Mzuzu kukakhala nawo pa maliro achibale ndipo pobwerera ndipamene wachita ngozi.
Noel Chikoleka, kapena kuti Phyzix, yemwe watsimikiza zaimfayi, wati ndi wosweka mtima ndipo dziko la Malawi lataya katakwe.
“Zikundivuta kumvetsa. Uyu anali mzanga ndipo ndayimba naye nyimbo zochuluka kuphatikizapo ‘Legend’ komanso ‘mkazi ‘uli fine’,” wadandaula Phyzix.
Spiral Mwenya wapambanapo mphoto zochuluka za Maso Awards pa luso lake la Graphic Designing.