Malawi Broadcasting Corporation
Development Health Local Local News Nkhani

Boma lati dziko lino silikuchita bwino pankhani zaukhondo

M’modzi mwa adindo ku unduna woona za madzi ndi zaukhondo, a Alexander Mwangonde, ati dziko la Malawi silikuchita bwino pa nkhani zaukhondo, zimene zikupereka chiopysezo ku matenda.

A Mwangonde anati matendawa ndi monga kolera komanso ena.

Iwo anati mwa mabanja 100 aliwonse, mabanja 49 okha ndi amene amakwanitsa kutsatira njira zoyenera zaukhondo monga kusamba m’manja pafupipafupi komanso kusamala zinyalala.

A Mwangonde amayankhula izi pa kanema wa wayilesi ya boma ya MBC munzinda wa Lilongwe pa mtsutso okhudza nkhani zaukhondo umene anthu osiyanasiyana, kuphatikizapo mafumu, akatswiri a zakafukufuku, akuluakulu a ku unduna wa zaumoyo komanso nzika, amakambirana momwe angathetsere mavutowa.

Mtsutsowu unakonzedwa ngati njira imodzi yofalitsira uthenga olimbikitsa anthu onse m’dziko muno kuti adziyika chidwi pankhani zaukhondo.

Nduna ya za madzi ndi ukhondo, a Abida Mia, anatsegulira sabata yolimbikitsa ukhondo pa 21 October chaka chino.

 

Print Friendly, PDF & Email

Related posts

Fire guts Zgambota rest house in Karonga, one Injured

MBC Online

Man Gets 12 Years IHL for Defilement

Alick Sambo

Artist crafts poem for First Lady

Romeo Umali
error: All Content is protected. Copyright © 2022. Malawi Broadcasting Corporation. All Right Reserved.