Alimi a ziweto a m’boma la Chikhwawa adandaula kaamba kakusagwira ntchito kwa malo osambitsako ziweto (dip), zomwe ati zikupereka chiopsyezo cha chigodola.
Izi zadziwika pamene bungwe la Catholic Development Commission (CADECOM) pamodzi ndi olembankhani anakayendera zina mwa zitukuko m’dera la mfumu yayikulu Ngabu m’bomalo.
Kumeneku amacheza ndi alimi komanso alangizi kuti adziwe za momwe zitukuko zikuyendera komanso mavuto omwe akukumana nawo.
M’modzi mwa alimiwa, a Mose Juga, amene amachokera kwa Senior Gulupu Jombo, anati akuvutika akafuna kuti asambitse ziweto zawo.
Pothilirapo ndemanga, mlangizi waziweto m’boma la Chikwawa, a Joseph Munyuma, avomereza za vutoli ndipo wati boma kudzera ku unduna wa zamalimidwe likuchita chotheka kuti malowa ayambenso kugwira ntchito.
Mlangizi wa CADECOM, a Aaron Kandiwo Mtaya, anati anatsogolera olembankhani ku malowa kuti adziwe zomwe akuchita polimbikitsa anthu a m’madera akumudzi kuti akhale ndi kuthekera koyankhula ndi adindo osiyanasiyana pa mavuto amene amakumana nawo pofuna kuwapezera mayankho.