Mtsogoleri wa dziko lino Dr Lazarus Chakwera m’mawa uno ali pa ulendo oyendera ntchito zachitukuko m’boma la Mangochi.
Dr Chakwera akuyembekezeka kuyendera komanso kucheza ndi anthu ogwira ntchito zokopa alendo ndipo ena mwa malowa ndi a Rosalyn’s Beach Hotel.
Dr Chakwera ayenderanso kampani yopanga cement ya Cement Products Limited ku Njereza ndipo akatero akayendera malo antchito zokopa alendo a Club Makokola komwenso akacheze ndi ogwira ntchito zamalonda.
Olemba: Owen Mavula