Chinthuzi : Football Association of Malawi
Anthu wokonda masewero a mpira wamiyendo m’dziko muno atsindika zakufunika koti oyimbira masewerowa agwire ntchito yawo mwaukadaulo pofuna kuti mpikisano wa TNM Super League wa chaka chino ukhale wapamwamba.
Mwa zina, anthuwa apempha woyimbirawa kuti asamawonetse kukondera timu iliyonse pomwe masewero akuchitika.
Popereka maganizo awo mu programme ya The Pot pa MBC, ambiri mwa anthuwa ati zakhala zili zodandaulitsa pomwe ena mwa oyimbirawa akhala akumalephera kupereka ziganizo zoyenera pa masewero ena, zomwenso zikumasokoneza mipikisano monga zinaliri chaka chatha.
Mpikisano wa TNM Super League uyambika kumapeto a sabata ino.
Timu FCB Nyasa Big Bullets, yomwe idali akatswiri a mpikisanowu chaka chapitachi, yagonjetsa timu ya Silver Strikers loweruka lapitali ndikutenganso chikho cha Charity Shield chomwe matimu amalimbirana kumayambiliro a a ligi.