Bungwe la Oxfam lati lalandira K650 million yoti igwire ntchito yothandizira ndondomeko yolimbikitsa amayi kutenga nawo gawo pandale.
Mkulu wa bungweli a Lingalireni Mihowa, wanena izi ku Lilongwe pomwe amasainirana ndi unduna owona zoti pasamakhale kusiyana pakati pa amayi ndi abambo.
A Mihowa ati kudzera mundondomeko ngati yomweyi mu chaka cha 2019 kwanthawi yoyamba anakwanitsa kupezetsa aphungu anayi m’boma la Mangochi ndipo ati ulendo uno chidwi aika m’maboma awiri, Nkhotakota ndi Mangochi.
“Tili ndi umboni kuti ntchitoyi ili ndi phindu. Taonjezerapo boma la Nkhotakota kaamba koti pakadali pano kulibeko phungu wachizimayi,” anatero a Mihowa.
M’mawu ake nduna yoona zakuti pasakhale kusiyana pakati pa amayi ndi abambo a Jean Sendeza ati ndiokondwa kaamba koti zomwe likupanga bungweli zikugwirizana ndi masomphenya a mtsogoleri wa dziko lino Dr Lazarus Chakwera otukula amayi.