Malawi Broadcasting Corporation
Nkhani

A Malawi adekhe pamene boma likumanganso misewu yolimba – Hara

A Jacob Hara, omwe ndi nduna ya za mtengamtenga, apempha anthu m’dziko muno kuti akhale odekha pamene boma likuyesetsa kukonzanso misewu.

Ndunayi yayakhula izi pomwe imayendera ntchito yomanga komaso kukonza msewu wa M1, kuchoka pa mphambano yopita ku Kamuzu International Airport ku Lilongwe kufika ku Kasungu mpaka kwa Jenda.

A Hara ati ndiokhutira ndi momwe ntchito yomanga msewuyi ikuyendera.

Mmodzi mwa akuluakulu ku Roads Authority, Engineer Joe Longwe, ati akulondoloza bwino lomwe nthawi yomwe anapatsana ndi ma kontrakitala omanga misewu ndi cholinga choti misewu ikhale yapamwamba.

Related posts

Olembankhani ndi mlatho wazochitika ku nyumba ya malamulo — CSAT

Romeo Umali

NEEF yakhazikitsa ngongole ya ulimi wa mthilira

Mayeso Chikhadzula

TNM ipereka mabandulo aulere kwa makasitomala ake popilira kuvuta kwa internet

Romeo Umali
error: All Content is protected. Copyright © 2022. Malawi Broadcasting Corporation. All Right Reserved.