Kampani ya zomangamanga ya SICO Holdings yayamikira a New Dawn Boxing Promotion, amene akuti amapereka malipoto abwino akalandira thandizo la ndalama.
Mkulu wa kampaniyi, a Mathews Mughogho, anena izi ku Lilongwe pamene amapereka K7.5 Million zothandizira nkhonya yomwe ichitike munzindawu loweruka likudzali pakati paHannock Phiri, yemwe ndi wakuno ku Malawi koma amakhala ku South Africa ndi Regen Champion wa ku Democratic Republic of Congo.
A Mughogho ati ndiochilimika kuthandiza pa zamasewero mdziko muno.
M’mawu ake, mmodzi mwa akuluakulu a New Dawn Boxing Promotion, a Brighton Mwando, wati thandizoli labwera munthawi yake ndipo ati liwathandiza kulipira osewera komanso amene akuthandizira kuyendetsa nawo nkhonyayi.
Iye watinso anthu ayembekeze kudzaona zapamwamba ati poti chilichonse achikonza mwadongosolo.